PHILADEPHIA CHURCH GETS ORGANISED

#emcnews
MPINGO WA PHILADELPHIA NCHIGAWO CHA SOUTH LUNZU TSOPANO NDIOLINGANIZIDWA

Tsiku la pa 23 March 2025 lidzakhala losaiwalika kwa akhristu ampingo wa Philadelphia nchigawo cha South Lunzu ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre pomwe tsopano awulinganiza. Izi zikutanthauza kuti azichita zinthu zonse paokha monga kudya mgonero komanso kupanga ziganizo mwa iwo okha posadalira kholo lawo.Mpigowu omwe unatsegulidwa pa 14 September 2024 ndi akhristu 105 tsopano uli ndi akhristu obatizidwa oposa 200. Mpingo wa Philadelphia unali wa mwana wa Nangafuwe 1.

Potsegulira mwambowu omwe unayamba ndi ya Khristu Mu Nyimbo 195, abusa achigawo cha South Lunzu, a Beaton S Kathumba ayamika likulu la mpingo nchigawo chakummawa chifukwa chizachitira umboni pakukula kwa nthambi ya Philadelphia. “Tikuthokoza akulu athu omwe abwera ndipo atilimbikitsa. Maloto a pano omwe abusa a Shadrach Msuka komanso Evangelist Dr Ernest Kaonga anali nawo apherezera okhala ndi mpingo chigawo chino” Anatero abusa a Kathumba.

Mau ake pomwe amalinganiza mpingowu, mlembi wa abusa komanso mkululu owona za udindo wachikhristu ku Eastern Malawi Conference, m’busa Benson L Mbewe walimbikitsa akhristu kuti achilimike komanso kupewa ziphunzitso zachilendo. “Monga mpingo tili ndi zomwe timakhulupilira molingana ndi Buku Lopatulika choncho ndawandaulira kuti asachite mosemphana”. Anayankhula m’busa B L Mbewe

Mwazina, lero pamwambowu akumbutsa zikhulupiliro za mpingo, adya mgonero komanso kusankha adindo oyendetsa mpingo ama department osiyanasiyana kuphatikizapo akulu ampingo.

Ena mwa alendo omwe anali nawo kumwambowu ndi mafumu atatu ozungulira derali, Evangelist Dr Ernest Kaonga ndi ena ambiri.

Wolemba : McAllan Mapinda
EMC Media

Leave a Comment

Your email address will not be published. Required fields are marked *