BUNGWE LA ACHINYAMATA NCHIGAWO CHAKU M'MAWA LIKHADZIKITSA NTCHITO ZACHIFUNDO
Bungwe la achinyamata mu mpingo wa Seventh Day Adventist m’chigawo cha kum’mawa pa 3 March 2025 lakhazikitsa ntchito zachifundo mu ndondomeko ya Global Youth Day (GYD) ya chaka chino.
Mwambowu omwe wachitikira pa sukulu ya ana aulumali osaona ya Nkope, ku Monkey Bay m’boma la Mangochi, unali opatsa chikoka chifukwa mwazina kunali nyimbo, ulaliki komanso kucheza ndi ophunzira ndi akuluakulu apa sukulupo.
Poyankhula, mtsogoleri wa achinyamata nchigawo cha Eastern Malawi Conference (EMC) , SYL M’busa Eanerst Kefa wati iyi ndi imodzi mwa ntchito zina zomwe bungwe la achinyamata limagwira mumpingo pothandiza komanso kusamalira anthu osowa munjira zosiyanasiyana. Iye anati apa tsopano ndiye kuti akhadzitsa ndondomeko ya ntchito zachifundozi yomwe tsopano ifikire nzigawo za m’ma Zone onse m’maboma asanu ndi limodzi omwe ali pansi pa EMC kuchigawo chaku m’awa.
Poyankhula atalandira thandizo lomwe achinyamatawo anabweretsa, m’modzi mwa akuluakulu a sukuluyi a Martin Mzikuola ayamika achinyamatawa ndi utsogoleri wa Eastern Malawi Conference kamba ka thandizoli ponena kuti lafika munthawi yake.
Mwazina bungwe la achinyamatawo lathandiza ndi katundu monga chimanga, sopo, mapepala wolemberapo anthu a ulumali osaona, mafuta odzola anthu achi albino komanso , mafuta wophikira ndi katundu wina osiyanasiyana.
Paulendowu panali achinyamata ochokera nzigawo za ma Zone amu EMC, Mtsogoleri wa Mpingo wa Seventh-day nchigawo chakummawa m’busa Dr Sanned Lubani, mkulu wa achinyamata nchigawochi m’busa Earnest Kefa, wapampando wa achinyamatawa SYL Vitumbiko Chijere Chirwa komanso mkulu owona zachuma Elder David Chipungu ku EMC mwa ena.